Tea Association of Malawi (TAML) Buku lophunzitsira ndondomeko zopewera nkhanza ndi zitonzo zochitika pa malo ogwira ntchito

Policy document

Ili ndi bukhu lophunzitsira za kapewedwe ka nkhanza ndi chitonzo pa malo a ntchito. Bukhuli linakhazikitsidwa mothandizidwa ndi bungwe lowona za ogwira ntchito pa dziko lonse la pansi (ILO) komanso TAML. Ndipo TAML imatsatira mfundo za ILO (C190)-Violence and Harassment Convention, 2019 (No. 190) powonetsetsa kuti pamalo pamene anthu akugwirapo ntchito ndi pabwino. Limalimbikitsa kuwonetsetsa kuti palibe kusiyana pakati pa amuna ndi akazi pogwira ntchito za malonda a mbewu ya Tea. TAML ndi ILO akugwira ntchito yothana ndi nkhanza mu malonda a tea. Zina mwa zomwe amachita ndi kuthetsa kusalana, kulimbikitsa kuti ogwira ntchito ali ndi zodzitetezera pogwira ntchito, kuthetsa nkhanza zosiyanasiyana.

Pofuna kukwaniritsa zimenezi TAML mu 2017 inakhazikitsa mfundo zolimbana ndi nkhanza, kusalana, chitetezo pa malo a ntchito, kusasalana potengera kuti wina ndi wa mwamuna kapena mkazi, ndipo mamembala onse a TAML anagwirizana nazo.
Izi zikugwirizana ndi malamulo a kusasiyana pakati pa amuna ndi akazi omwe anakhazikitsidwa m’chaka cha 2015 komanso kuthandizira malingaliro a bungwe la Malawi Human Rights Commission (MHRC) lomwe limawonetsetsa kuti mabungwe akutsatira mfundo za kusasiyana pakati pa amuna ndi akazi popanga malamulo awo.
Bukhu lophunzitsirali likukwaniritsa malingaliro a MHRC.TAML ndi ILO amakhulupilira kuti maphunziro angathandizire kuzindikiritsa anthu zinthu zomwe zingathandize kuthana ndi nkhanza kapena kusalana pa malo a ntchito. Kusula anthu kuthandiziranso kulimbana ndi mavutowa mu ntchito ya tea.
Bukhuli linakhazikitsidwa potsatira madandaulo omwe akhala akupezeka mu ntchito za tea komanso kufunika kochitapo kanthu polimbana ndi madandaulowa. Pothana ndi mavutowa TAML ndi ILO amathandizira kuzindikiritsa anthu za kufunika kokhala ndi malo ogwirira ntchito otetezeka komanso abwino.