Malawi Congress of Trade Union (MCTU) Ndondomeko Zoonetsetsa Kuti Pasakhale Kusiyana Pakati Pa Amayi Ndi Abambo Komanso Kuchitirana Nkhanza Zosiyanasiyana Pamalo Antchito
Policy document
Kuyambira nthawi imene bungwe la Malawi Congress of Trade Union linakhazikitsa ndondomeko zokhudza kuthana kuchitirana nkhanza pamalo anchito mchaka cha 2022 komanso ndondomeko zoona kuti pasamakhale kusiyana kwa pakati pa akazi ndi amuna mmalo antchito mu 2017, zambiri zachitika. A Malawi ambiri ogwira ntchito, akupitilira kusalidwa komanso kuchitiridwa nkhanza zosiyanasiyana kuphatikizapo zokhudza kugonana potengera kuti iwo ndi aakazi kapena aamuna. Nkhanzazi zimachitika pamene anthuwa akufuna kulowa nchito, pamene ali pantchito ngakhalenso pamene akufuna kusiya ntchito.
Ichi nchifukwa chake bungwe la MCTU laganiza zounikiranso ndikuyika pamodzi ndondomeko zoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pantchito zomwe zinakonzedwa muchaka cha 2017 ndi ndondomeko zopititsa patsogolo ntchito yoona kuti ogwira ntchito onse sakuchitiridwa nkhanza zomwe zinakonzedwa mu chaka cha 2022. Ndondomeko zophatikizazi zapangidwa ndicholinga choti bungwe la MCTU lionetse chidwi chake pofuna kupereka malo ogwirira ntchito otetezeka kwa ogwira ntchito ake ku bungweli komanso ku nthambi zake zonse.
Bungwe la Malawi Congress of Trade Union likufuna kuthokoza bungwe lakunja lowona za anthu ogwira ntchito chifukwa cha chithandizo cha ndalama chomwe chinapangitsa kuti ndondomekozi zilembedwe. Nkhani zikulu zikulu zomwe zalembedwa mu ndondomekoyi zithandizira kwambiri pofuna kuunika ndondomeko zokhudza kusiyana pakati pa amayi ndi abambo komanso chitonzo pankhani zogonana zomwe amayi ndi abambo amachitirana mmalo awo ogwirira ntchito.
Additional details
Author(s)
- Malawi Congress of Trade Unions (MCTU)